×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 150

1
Haleluya, Lemekezani Mulungu m'malo ace oyera; Mlemekezeni m'thambo la mphamvu yace.
2
Mlemekezeni cifukwa ca nchito zace zolimba; Mlemekezeni monga mwa ukulu wace waunjinji.
3
Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; Mlemekezeni ndi cisakasa ndi zeze.
4
Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoyimbira za zingwe ndi citoliro.
5
Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa.
6
Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Haleluya.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba