Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Mikitamu ya Davide. Ndisungeni Inu Mulungu, pakuti ine ndimathawira kwa Inu. |
| 2 |
| Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga; popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.” |
| 3 |
| Kunena za oyera mtima amene ali pa dziko, amenewa ndi olemekezeka, amene ndimakondwera nawo. |
| 4 |
| Anthu amene amathamangira kwa milungu ina mavuto awo adzachulukadi. Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga. |
| 5 |
| Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa; mwateteza kolimba gawo langa. |
| 6 |
| Malire a malo anga akhala pabwino; ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri. |
| 7 |
| Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu; ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza. |
| 8 |
| Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. |
| 9 |
| Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera; thupi langanso lidzakhala pabwino, |
| 10 |
| chifukwa Inu simudzandisiya ku manda, simudzalola kuti woyera wanu avunde. |
| 11 |
| Inu mwandidziwitsa njira ya moyo; mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu, ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/016.mp3
150
16