Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Yehova, imvani cilungamo, mverani mpfuu wanga; Cherani khutu ku pemphero langa losaturuka m'milomo ya cinyengo, |
| 2 |
| Pankhope panu paturuke ciweruzo canga; Maso anu apenyerere zolunjika, |
| 3 |
| Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; Mwandisuntha, simupeza kanthu; Ndatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa. |
| 4 |
| Za macitidwe a anthu, ndaceniera ndi mau a milomo yanu Ndingalowe njira za woononga. |
| 5 |
| M'mayendedwe anga ndasunga mabande anu, Mapazi anga sanaterereka. |
| 6 |
| Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu: Cherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga. |
| 7 |
| Onetsani cifundo canu codabwiza, Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu Kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja. |
| 8 |
| Ndisungeni monga kamwana ka m'diso, Ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu, |
| 9 |
| Kundilanditsa kwa oipa amene andipasula, Adani a pa moyo wanga amene andizinga. |
| 10 |
| Mafuta ao awatsekereza; M'kamwa mwao alankhula modzikuza. |
| 11 |
| Tsopano anatizinga m'mayendedwe athu: Apenyetsetsa m'maso kuti atigwetse pansi. |
| 12 |
| Afanana ndi mkango wofuna kumwetula, Ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo. |
| 13 |
| Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse: Landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu; |
| 14 |
| Kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, Kwa anthu a dziko lapansi pano amene colowa cao ciri m'moyo uno, Ndipo mimba yao muidzaza ndi cuma canu cobisika: Akhuta mtima ndi ana, Nasiyira ana amakanda zocuruka zao. |
| 15 |
| Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'cilungamo: Ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/017.mp3
150
17