×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 19

1
Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; Ndipo thambo lionetsa nchito ya manja ace.
2
Usana ndi usana ucurukitsa mau, Ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.
3
Palibe cilankhulidwe, palibe mau; Liu lao silimveka.
4
Muyeso wao wapitirira pa dziko lonse lapansi, Ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu. Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,
5
Ndipo liri ngati mkwati wakuturuka m'cipinda mwace, Likondwera ngati ciphona kuthamanga m'njira.
6
Kuturuka kwace lituruka kolekezera thambo, Ndipo kuzungulira kwace lifikira ku malekezero ace: Ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwace.
7
Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; Mboni za Yehova ziri zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru;
8
Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima: Malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
9
Kuopa Yehova kuli mbe, kwakukhalabe nthawi zonse: Maweruzo a Yehova ali oona, alungama konse konse.
10
Ndizo zifunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa: Zizuna koposa uci ndi zakukha za zisa zace,
11
Ndiponso kapolo wanu acenjezedwa nazo: M'kuzisunga izo muli mphotho yaikuru.
12
Adziwitsa zolowereza zace ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika.
13
Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; Zisacite ufumu pa ine: pamenepo ndidzakhala wangwiro, Ndi wosacimwa colakwa cacikuru.
14
Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga abvomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga,
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba