Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu? Akonzekeranji zopanda pake anthu? |
| 2 |
| Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo. |
| 3 |
| Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo ndipo titaye zingwe zawo.” |
| 4 |
| Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo. |
| 5 |
| Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti, |
| 6 |
| “Ine ndakhazikitsa mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.” |
| 7 |
| Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula: Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga; lero Ine ndakhala Atate ako. |
| 8 |
| Tandipempha, ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako; malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako. |
| 9 |
| Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo; udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.” |
| 10 |
| Kotero, inu mafumu, chenjerani; chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi. |
| 11 |
| Tumikirani Yehova mwa mantha ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera. |
| 12 |
| Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/002.mp3
150
2