Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Yehova akubvomereze tsiku la nsautso; Dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje; |
| 2 |
| Likutumizire thandizo loturuka m'malo oyera, Ndipo likugwirizize kucokera m'Ziyoni; |
| 3 |
| Likumbukile zopereka zako zonse, Lilandire nsembe yako yopsereza; |
| 4 |
| Likupatse ca mtima wako, Ndipo likwaniritse upo wako wonse. |
| 5 |
| Tidzapfuula mokondwera mwa cipulumutso canu, Ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera: Yehova akwaniritse mapempho ako onse. |
| 6 |
| Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wace; Adzambvomereza m'Mwamba mwace moyera Ndi mphamvu ya cipulumutso ca dzanja lace lamanja. |
| 7 |
| Ena atama magareca, ndi ena akavalo: Koma ife tidzachula dzina la Yehova Mulungu wathu. |
| 8 |
| Iwowa anagonieka, nagwa: Koma ife tauka, ndipo takhala ciriri. |
| 9 |
| Yehova, pulumutsani, Mfumuyo atibvomereze tsiku lakuitana ife. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/020.mp3
150
20