Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu; Adzakondwera kwakukuru m'cipulumutso canu! |
| 2 |
| Mwampatsa iye cikhumbo ca mtimawace, Ndipo simunakana pempho la milomo yace. |
| 3 |
| Pakuti mumkumika iye ndi madalitso okoma: Muika korona wa golidi woyengetsa pamutu pace. |
| 4 |
| Anakupemphani moyo, mwampatsa iye; Mwamtalikitsira masiku ku nthawi za nthawi. |
| 5 |
| Ulemerero wace ngwaukuru mwa cipulumutso canu: Mumcitira iye ulemu ndi ukulu. |
| 6 |
| Pakuti mumuikira madalitso ku nthawi zonse; Mumkondweretsa ndi cimwemwe pankhope panu. |
| 7 |
| Pakuti mfumu akhulupirira Yehova, Ndipo mwa cifundo ca Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye, |
| 8 |
| Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse: Dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu. |
| 9 |
| Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu. Yehova adzawatha m'kukwiya kwace, Ndipo moto udzawanyeketsa. |
| 10 |
| Mudzaziononga zobala zao kuzicotsa pa dziko lapansi, Ndi mbeu zao mwa ana a anthu. |
| 11 |
| Pakuti anakupangirani coipa: Anapangana ciwembu, osakhoza kucicita. |
| 12 |
| Pakuti mudzawabweza m'mbuyo, Popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao, |
| 13 |
| Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu: Potero tidzayimba ndi kulemekeza cilimbiko canu. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/021.mp3
150
21