Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo la Davide. Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo, dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo; |
| 2 |
| pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja ndi kulikhazika pamwamba pa madzi. |
| 3 |
| Ndani angakwere phiri la Yehova? Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika? |
| 4 |
| Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera, amene sapereka moyo wake kwa fano kapena kulumbira mwachinyengo. |
| 5 |
| Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu. |
| 6 |
| Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova; amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo. Sela |
| 7 |
| Tukulani mitu yanu inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe. |
| 8 |
| Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo. |
| 9 |
| Tukulani mitu yanu, inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe. |
| 10 |
| Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Iye ndiye Mfumu yaulemerero. Sela |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/024.mp3
150
24