|
| 1 |
|
| Ndikweza moyo wanga kwa Inu, Yehova. |
|
| 2 |
|
| Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu, Ndisacite manyazi; Adani anga asandiseke ine. |
|
| 3 |
|
| Inde, onse akuyembekezera Inu sadzacita manyazi Adzacita manyazi iwo amene acita monyenga kopanda cifukwa. |
|
| 4 |
|
| Mundidziwitse njira zanu, Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu. |
|
| 5 |
|
| Munditsogolere m'coonadi canu, ndipo mundiphunzitse; Pakuti Inu ndinu Mulungu wa cipulumutso canga; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli. |
|
| 6 |
|
| Kumbukilani, Yehova, nsoni zanu ndi cifundo canu; Pakuti izi nza kale lonse, |
|
| 7 |
|
| Musakumbukile zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu: Mundikumbukile monga mwa cifundo canu, Cifukwa ca ubwino wanu, Yehova. |
|
| 8 |
|
| Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima: Cifukwa cace adzaphunzitsa olawa za njira. |
|
| 9 |
|
| Adzawatsogolera ofatsa m'ciweruzo: Ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yace. |
|
| 10 |
|
| Mayendedwe onse a Yehova ndiwo cifundo ndi coonadi, Kwa iwo akusunga pangano lace ndi mboni zace. |
|
| 11 |
|
| Cifukwa ca dzina lanu, Yehova, Ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukuru. |
|
| 12 |
|
| Munthuyo wakuopa Yehova ndani? Adzamlangiza iye njira adzasankheyo. |
|
| 13 |
|
| Moyo wace udzakhala mokoma; Ndi mbumba zace zidzalandira dziko lapansi. |
|
| 14 |
|
| Cinsinsi ca Yehova ciri kwa iwo akumuopa Iye; Ndipo adzawadziwitsa pangano lace. |
|
| 15 |
|
| Maso anga alinga kwa Yehova kosaleka; Pakuti Iye adzaonjola mapazi anga m'ukonde. |
|
| 16 |
|
| Ceukirani ine ndipo ndicitireni cifundo; Pakuti ndiri woungumma ndi wozunzika. |
|
| 17 |
|
| Masautso a mtima wanga akula: Munditurutse m'zondipsinja. |
|
| 18 |
|
| Penyani mazunzo anga ndi zabvuta zanga; Ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse. |
|
| 19 |
|
| Penyani adani anga, popeza acuruka; Ndipo andida ndi udani waciwawa. |
|
| 20 |
|
| Sungani moyo wanga, ndilanditseni, Ndisakhale nao manyazi, pakuti ndakhulupirira Inu. |
|
| 21 |
|
| Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge, Pakuti ndayembekezera Inu. |
|
| 22 |
|
| Ombolani Israyeli, Mulungu, M'masautso ace onse. |
|
|
|
|