|
| 1 |
|
| Salimo la Davide. Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga. |
|
| 2 |
|
| Ndimadalira Inu Mulungu wanga. Musalole kuti ndichite manyazi kapena kuti adani anga andipambane. |
|
| 3 |
|
| Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye sadzachititsidwa manyazi koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera. |
|
| 4 |
|
| Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova, phunzitseni mayendedwe anu; |
|
| 5 |
|
| tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa, pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga, ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse. |
|
| 6 |
|
| Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu, pakuti ndi zakalekale. |
|
| 7 |
|
| Musakumbukire machimo a ubwana wanga ndi makhalidwe anga owukira; molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine, pakuti Inu Yehova ndinu wabwino. |
|
| 8 |
|
| Yehova ndi wabwino ndi wolungama; choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake. |
|
| 9 |
|
| Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama ndipo amawaphunzitsa njira zake. |
|
| 10 |
|
| Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake. |
|
| 11 |
|
| Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova, khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka. |
|
| 12 |
|
| Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova? Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate. |
|
| 13 |
|
| Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse, ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo. |
|
| 14 |
|
| Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa; amawulula pangano lake kwa iwowo. |
|
| 15 |
|
| Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse, pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha. |
|
| 16 |
|
| Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima, pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika. |
|
| 17 |
|
| Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira; masuleni ku zowawa zanga. |
|
| 18 |
|
| Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga ndipo mufafanize machimo anga onse. |
|
| 19 |
|
| Onani mmene adani anga achulukira ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira. |
|
| 20 |
|
| Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa; musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndimathawira kwa Inu. |
|
| 21 |
|
| Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze, chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu. |
|
| 22 |
|
| Wombolani Israeli Inu Mulungu, ku mavuto ake onse! |
|
|
|
|