|
| 1 |
|
| Yehova ndiye kuunika kwanga ndi cipulumutso canga; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzacita mantha ndi yani? |
|
| 2 |
|
| Pondifika ine ocita zoipa kudzadya mnofu wanga, Inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa. |
|
| 3 |
|
| Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole, Mtima wanga sungacite mantha: Ingakhale nkhondo ikandiukira, Nde pomweponso ndidzakhulupira, |
|
| 4 |
|
| Cinthu cimodzi ndinacipempha kwa Yehova, ndidzacilondola ici: Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, Kupenya kukongola kwace kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kacisi wace. |
|
| 5 |
|
| Cifukwa kuti pa dzuwa la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwace: Adzandibisa m'tsenjezi mwa cihema cace; Pathanthwe adzandikweza. |
|
| 6 |
|
| Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga; Ndipo ndidzapereka m'cihema mwace nsembe za kupfuula mokondwera; Ndidzayimba, inde, ndidzayimbira Yehova zomlemekeza. |
|
| 7 |
|
| Imvani, Yehova, liu langa popfuula ine: Mundicitirenso cifundo ndipo mundibvomereze. |
|
| 8 |
|
| Pamene munati, Punani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu: Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna. |
|
| 9 |
|
| Musandibisire ine nkhope yanu; Musacotse kapolo wanu ndi kukwiya: Inu munakhala thandizo langa; Musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa cipulumutso canga, |
|
| 10 |
|
| Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga, Koma Yehova anditola. |
|
| 11 |
|
| Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, Munditsogolere pa njira yacidikha, Cifukwa ca adani anga, |
|
| 12 |
|
| Musandipereke ku cifuniro ca akundisautsa; Cifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zaciwawa. |
|
| 13 |
|
| Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova M'dziko la amoyo, ndikadatanil |
|
| 14 |
|
| Yembekeza Yehova: Limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; Inde, yembekeza Yehova. |
|
|
|
|