Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo la Davide. Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa; musakhale osamva kwa ine. Pakuti mukapitirira kukhala chete, ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje. |
| 2 |
| Imvani kupempha chifundo kwanga pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize, pomwe ndikukweza manja anga kuloza ku malo anu oyeretsetsa. |
| 3 |
| Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa, pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa, amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo. |
| 4 |
| Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo ndi ntchito zawo zoyipa; abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera. |
| 5 |
| Popeza iwowo sakhudzidwa ndi ntchito za Yehova, ndi zimene manja ake anazichita, Iye adzawakhadzula ndipo sadzawathandizanso. |
| 6 |
| Matamando apite kwa Yehova, popeza Iye wamva kupempha chifundo kwanga. |
| 7 |
| Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa. Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo. |
| 8 |
| Yehova ndi mphamvu ya anthu ake, linga la chipulumutso kwa wodzozedwa wake. |
| 9 |
| Pulumutsani anthu anu ndipo mudalitse cholowa chanu; mukhale mʼbusa wawo ndipo muwakweze kwamuyaya. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/028.mp3
150
28