Buku Loyera
|
| 1 |
| Ndikuitana Inu Chauta, Inu thanthwe langa, musachite ngati simukundimva, chifukwa ngati mukhala chete, ndidzafanafana ndi anthu otsikira ku manda. |
| 2 |
| Imvani kupempha kwanga, pamene ndikulirira Inu kuti mundithandize, pamene ndikukupembedzani pokweza manja anga ku malo anu opatulika kopambana. |
| 3 |
| Musandichotsere kumodzi ndi anthu oipa, anthu amene amachita zonyenga, amene amalankhula zamtendere ndi anzao, koma mitima yao ndi yodzaza ndi chidani. |
| 4 |
| Muŵabwezere anthu otere molingana ndi ntchito zao, muŵalange molingana ndi zoipa zimene ankachita. Muŵabwezere molingana ndi ntchito zao, Muŵalange molingana ndi kuipa kwa ntchito zao. |
| 5 |
| Chifukwa chakuti iwo sasamalako ntchito za Chauta, ngakhale zimene adalenga Iye. Chauta adzaŵagumula ngati nyumba, osaŵamanganso. |
| 6 |
| Chauta atamandike, pakuti wamva liwu la kupempha kwanga. |
| 7 |
| Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga. |
| 8 |
| Chauta ndiye mphamvu zimene anthu ake amadalira, ndiye kothaŵira komwe wodzozedwa wake amapulumukirako. |
| 9 |
| Pulumutsani anthu anu, Inu Chauta, mudalitse amene mudaŵasankha. Mukhale mbusa wao, muŵasamale mpaka muyaya. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/028.mp3
150
28