Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo la Davide. Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu. |
| 2 |
| Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake, pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake. |
| 3 |
| Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi; Mulungu waulemerero abangula, Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu. |
| 4 |
| Liwu la Yehova ndi lamphamvu; liwu la Yehova ndi laulemerero. |
| 5 |
| Liwu la Yehova limathyola mikungudza; Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni. |
| 6 |
| Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe, Siriyoni ngati mwana wa njati: |
| 7 |
| Liwu la Yehova limakantha ngati kungʼanima kwa mphenzi. |
| 8 |
| Liwu la Yehova limagwedeza chipululu; Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi. |
| 9 |
| Liwu la Yehova limapindapinda mibawa ndi kuyeretsa nkhalango. Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!” |
| 10 |
| Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira, Yehova ndiye mfumu kwamuyaya. |
| 11 |
| Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake; Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/029.mp3
150
29