Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu. Inu Yehova, achulukadi adani anga! Achulukadi amene andiwukira! |
| 2 |
| Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” Sela |
| 3 |
| Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula. |
| 4 |
| Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. Sela |
| 5 |
| Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza. |
| 6 |
| Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse. |
| 7 |
| Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa. |
| 8 |
| Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu. Sela |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/003.mp3
150
3