Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu. Ndidzakukwezani Yehova, chifukwa mwanditulutsa kwakuya, ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine. |
| 2 |
| Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa. |
| 3 |
| Inu Yehova, munanditulutsa ku manda, munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje. |
| 4 |
| Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika; tamandani dzina lake loyera. |
| 5 |
| Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa. |
| 6 |
| Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati, “Sindidzagwedezekanso.” |
| 7 |
| Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, munachititsa phiri langa kuyima chilili; koma pamene munabisa nkhope yanu, ndinataya mtima. |
| 8 |
| Kwa Inu Yehova ndinayitana; kwa Ambuye ndinapempha chifundo; |
| 9 |
| “Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga ngati nditsikira ku dzenje? Kodi fumbi lidzakutamandani Inu? Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu? |
| 10 |
| Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo; Yehova mukhale thandizo langa.” |
| 11 |
| Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina; munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe, |
| 12 |
| kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/030.mp3
150
30