Buku Loyera
|
| 1 |
| Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa. Simudalole kuti adani anga akondwere poona kuti ndikuvutika. |
| 2 |
| Chauta, Mulungu wanga, ndidalirira Inu kuti mundithandize, ndipo mwandichiritsa. |
| 3 |
| Inu Chauta, mwanditulutsa m'dziko la akufa, mwandibwezeranso moyo kuti ndingatsikire ku manda. |
| 4 |
| Imbani nyimbo zotamanda Chauta, inu anthu ake oyera mtima, mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera. |
| 5 |
| Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha. |
| 6 |
| Koma ine, pamene zinthu zidaandiyendera bwino, ndidati, “Sindidzagwedezeka konse.” |
| 7 |
| Chifukwa cha kukoma mtima kwanu, Inu Chauta, mudandikhazikitsa ngati phiri lolimba. Koma pamene mudandimana madalitso anu, ine ndidataya mtima. |
| 8 |
| Pamenepo ndidalirira Inu Chauta, ndipo ndidapempha chifundo chanu kuti, |
| 9 |
| “Kodi mudzapindulanji pa imfa yanga ngati nditsikira ku manda? Kodi ine nditasanduka fumbi, ndingathe kukutamandani? Kodi pamenepo ndingathe kulalika za kukhulupirika kwanu? |
| 10 |
| “Imvani, Inu Chauta, ndipo mundikomere mtima. Inu Chauta, mukhale mthandizi wanga.” |
| 11 |
| Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina, mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo. |
| 12 |
| Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/030.mp3
150
30