Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo la Davide. Malangizo. Ngodala munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa; amene machimo ake aphimbidwa. |
| 2 |
| Ngodala munthu amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo. |
| 3 |
| Pamene ndinali chete, mafupa anga anakalamba chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse. |
| 4 |
| Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu linandipsinja; mphamvu zanga zinatha monga nthawi yotentha yachilimwe. Sela |
| 5 |
| Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu, sindinabise mphulupulu zanga. Ndinati, “Ine ndidzawulula zolakwa zanga kwa Yehova, ndipo Inu munandikhululukira mlandu wa machimo anga.” Sela |
| 6 |
| Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo pomwe mukupezeka; ndithu pamene madzi amphamvu auka, sadzamupeza. |
| 7 |
| Inu ndi malo anga obisala; muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga ndi nyimbo zachipulumutso. Sela |
| 8 |
| Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira. |
| 9 |
| Usakhale ngati kavalo kapena bulu, zimene zilibe nzeru, koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu, ukapanda kutero sizibwera kwa iwe. |
| 10 |
| Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa koma chikondi chosatha cha Yehova chimamuzinga munthu amene amadalira Iye. |
| 11 |
| Kondwerani mwa Yehova inu olungama; imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima! |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/032.mp3
150
32