Buku Loyera
|
| 1 |
| Ngwodala amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene machimo ake afafanizidwa. |
| 2 |
| Ngwodala amene Chauta samuŵerengera mlandu wake, amene mumtima mwake mulibe zonyenga. |
| 3 |
| Pamene ndinali ndisanaulule tchimo langa, thupi langa linali lofooka, chifukwa cha kubuula tsiku lonse. |
| 4 |
| Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu lidandipsinja, motero nyonga zanga zidatha, monga amafotera masamba ndi dzuŵa lachilimwe. |
| 5 |
| Koma ndidavomera tchimo langa kwa Inu, sindidabise kuipa kwanga. Ndidati, “Ndidzaulula machimo anga kwa Chauta,” pomwepo Inu mudakhululukiradi mlandu wa machimo anga. |
| 6 |
| Nchifukwa chake munthu aliyense wosamala za Inu apemphere kwa Inu. Akadzafika mavuto, akadzafika madzi a chigumula, zonsezo sizidzamufika. |
| 7 |
| Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu. |
| 8 |
| Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira. |
| 9 |
| “Musakhale opanda nzeru ngati kavalo kapena bulu amene ayenera kumuwongolera ndi chitsulo cham'kamwa ndi chapamutu, chifukwa ukapanda kutero, nyamazo sizidzakumvera.” |
| 10 |
| Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri, koma munthu wokhulupirira Chauta amazingidwa ndi chikondi chosasinthika. |
| 11 |
| Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/032.mp3
150
32