|
| 1 |
|
| Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama, nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo. |
|
| 2 |
|
| Mutamandeni Yehova ndi pangwe; muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi. |
|
| 3 |
|
| Muyimbireni nyimbo yatsopano; imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe. |
|
| 4 |
|
| Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona; Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita. |
|
| 5 |
|
| Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama; dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha. |
|
| 6 |
|
| Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa, zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake. |
|
| 7 |
|
| Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko; amayika zozama mʼnyumba zosungiramo. |
|
| 8 |
|
| Dziko lonse lapansi liope Yehova; anthu onse amulemekeze Iye. |
|
| 9 |
|
| Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo; Iye analamulira ndipo zinakhazikika. |
|
| 10 |
|
| Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina; Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri. |
|
| 11 |
|
| Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya, zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse. |
|
| 12 |
|
| Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova, anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake. |
|
| 13 |
|
| Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi ndi kuona anthu onse; |
|
| 14 |
|
| kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira onse amene amakhala pa dziko lapansi. |
|
| 15 |
|
| Iye amene amapanga mitima ya onse, amaona zonse zimene akuchita. |
|
| 16 |
|
| Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo; palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu. |
|
| 17 |
|
| Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso, ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa. |
|
| 18 |
|
| Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye; amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha, |
|
| 19 |
|
| kuwawombola iwo ku imfa ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala. |
|
| 20 |
|
| Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo; Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu. |
|
| 21 |
|
| Mwa Iye mitima yathu imakondwera, pakuti ife timadalira dzina lake loyera. |
|
| 22 |
|
| Chikondi chanu chosatha chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu. |
|
|
|
|