|
| 1 |
|
| Salimo la Davide. Pamene iye ananyengezera misala pamaso pa Abimeleki, amene anamupirikitsa, iyeyo nʼkuchoka. Ndidzayamika Yehova nthawi zonse; matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse. |
|
| 2 |
|
| Moyo wanga udzanyadira Yehova; anthu osautsidwa amve ndi kukondwera. |
|
| 3 |
|
| Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine; tiyeni pamodzi tikuze dzina lake. |
|
| 4 |
|
| Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha; anandilanditsa ku mantha anga onse. |
|
| 5 |
|
| Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira; nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi. |
|
| 6 |
|
| Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva; Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse. |
|
| 7 |
|
| Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye ndi kuwalanditsa. |
|
| 8 |
|
| Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino; wodala munthu amene amathawira kwa Iye. |
|
| 9 |
|
| Wopani Yehova inu oyera mtima ake, pakuti iwo amene amaopa Iye sasowa kanthu. |
|
| 10 |
|
| Mikango itha kulefuka ndi kumva njala koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino. |
|
| 11 |
|
| Bwerani ana anga, mundimvere; ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova. |
|
| 12 |
|
| Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri, |
|
| 13 |
|
| asunge lilime lake ku zoyipa ndi milomo yake kuti isayankhule zonama. |
|
| 14 |
|
| Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino; funafuna mtendere ndi kuwulondola. |
|
| 15 |
|
| Maso a Yehova ali pa olungama ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo; |
|
| 16 |
|
| nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa, kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi. |
|
| 17 |
|
| Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva; Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse. |
|
| 18 |
|
| Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu. |
|
| 19 |
|
| Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri, Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo, |
|
| 20 |
|
| Iye amateteza mafupa ake onse, palibe limodzi la mafupawo limene lidzathyoledwa. |
|
| 21 |
|
| Choyipa chidzapha anthu oyipa; adani a olungama adzapezeka olakwa. |
|
| 22 |
|
| Yehova amawombola atumiki ake; aliyense amene amathawira kwa Iye sadzapezeka wolakwa. |
|
|
|
|