|
| 1 |
|
| Ndidzayamika Chauta nthaŵi zonse, pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza. |
|
| 2 |
|
| Moyo wanga umanyadira Chauta. Anthu ozunzika amve ndipo akondwere. |
|
| 3 |
|
| Lalikani pamodzi nane ukulu wa Chauta, tiyeni limodzi tiyamike dzina lake. |
|
| 4 |
|
| Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha. Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa. |
|
| 5 |
|
| Ozunzikawo atayang'ana kwa Chauta, nkhope zao zidasangalala, sadachite manyazi. |
|
| 6 |
|
| Munthu wosaukayu adalira, ndipo Chauta adamumva, nampulumutsa m'mavuto ake onse. |
|
| 7 |
|
| Mngelo wa Chauta amatchinjiriza anthu omvera Iye, ndipo amaŵapulumutsa. |
|
| 8 |
|
| Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino. Ngwodala munthu wothaŵira kwa Chauta. |
|
| 9 |
|
| Muzimvera Chauta, inu anthu ake oyera mtima, pakuti amene amamumvera sasoŵa kanthu. |
|
| 10 |
|
| Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino. |
|
| 11 |
|
| Bwerani ana anga, mundimvere, ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta. |
|
| 12 |
|
| Ndani mwa inu amakhumba moyo ndi kulakalaka kuti akhale masiku ambiri, kuti asangalale ndi zinthu zabwino? |
|
| 13 |
|
| Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa, pakamwa pako pasakambe zonyenga. |
|
| 14 |
|
| Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino. Funafuna mtendere ndi kuulondola. |
|
| 15 |
|
| Ngati mumvera Chauta, adzakuyang'anirani ndipo adzayankha kupempha kwanu. |
|
| 16 |
|
| Koma Chauta amaŵakwiyira anthu ochita zoipa, anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano. |
|
| 17 |
|
| Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. |
|
| 18 |
|
| Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima. |
|
| 19 |
|
| Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse. |
|
| 20 |
|
| Chauta amasunga thupi la munthuyo, palibe fupa limene limasweka. |
|
| 21 |
|
| Choipa chitsata mwini, anthu odana ndi munthu wa Mulungu adzalangidwa. |
|
| 22 |
|
| Chauta amaombola moyo wa atumiki ake. Palibe wothaŵira kwa Iye amene adzalangidwe. |
|
|
|
|