|
| 1 |
|
| Salimo la Davide. Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa; |
|
| 2 |
|
| pakuti monga udzu iwo adzafota msanga, ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga. |
|
| 3 |
|
| Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino; khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika. |
|
| 4 |
|
| Udzikondweretse wekha mwa Yehova ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako. |
|
| 5 |
|
| Pereka njira yako kwa Yehova; dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi: |
|
| 6 |
|
| Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha, chiweruzo chako ngati dzuwa la masana. |
|
| 7 |
|
| Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa; usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo, pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa. |
|
| 8 |
|
| Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali, usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa. |
|
| 9 |
|
| Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa, koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko. |
|
| 10 |
|
| Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso; ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso. |
|
| 11 |
|
| Koma ofatsa adzalandira dziko ndipo adzasangalala ndi mtendere waukulu. |
|
| 12 |
|
| Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama ndipo amawakukutira mano; |
|
| 13 |
|
| koma Ambuye amaseka oyipa pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera. |
|
| 14 |
|
| Oyipa amasolola lupanga ndi kupinda uta kugwetsa osauka ndi osowa, kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama. |
|
| 15 |
|
| Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe, ndipo mauta awo anathyoka. |
|
| 16 |
|
| Zabwino zochepa zimene olungama ali nazo ziposa chuma cha anthu oyipa ambiri; |
|
| 17 |
|
| pakuti mphamvu ya oyipa idzasweka, koma Yehova amasunga olungama. |
|
| 18 |
|
| Masiku a anthu osalakwa amadziwika ndi Yehova, ndipo cholowa chawo chidzakhala mpaka muyaya. |
|
| 19 |
|
| Pa nthawi ya mavuto iwo sadzafota; mʼmasiku a njala adzakhala ndi zinthu zambiri. |
|
| 20 |
|
| Koma oyipa adzawonongeka; adani a Yehova adzakhala ngati kukongola kwa kuthengo, iwo adzazimirira ngati utsi. |
|
| 21 |
|
| Oyipa amabwereka ndipo sabweza koma olungama amapereka mowolowamanja. |
|
| 22 |
|
| Iwo amene Yehova amawadalitsa adzalandira dziko, koma amene Iye amawatemberera adzachotsedwa. |
|
| 23 |
|
| Ngati Yehova akondwera ndi njira ya munthu, amakhazikitsa mayendedwe ake; |
|
| 24 |
|
| ngakhale atapunthwa sadzagwa, pakuti Yehova amamutchinjiriza ndi dzanja lake. |
|
| 25 |
|
| Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba koma sindinaonepo olungama akusiyidwa kapena ana awo akupempha chakudya. |
|
| 26 |
|
| Iwo ndi owolowamanja nthawi zonse ndipo amabwereketsa mwaufulu; ana awo adzadalitsika. |
|
| 27 |
|
| Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino; pamenepo udzakhazikika mʼdziko kwamuyaya. |
|
| 28 |
|
| Pakuti Yehova amakonda wolungama ndipo sadzasiya okhulupirika ake. Iwo adzatetezedwa kwamuyaya, koma zidzukulu za oyipa zidzachotsedwa; |
|
| 29 |
|
| olungama adzalandira dziko ndipo adzakhazikikamo kwamuyaya. |
|
| 30 |
|
| Pakamwa pa munthu wolungama pamayankhula za nzeru, ndipo lilime lake limayankhula zolungama. |
|
| 31 |
|
| Lamulo la Mulungu wake lili mu mtima mwake; mapazi ake saterereka. |
|
| 32 |
|
| Oyipa amabisala kudikira olungama; kufunafuna miyoyo yawoyo; |
|
| 33 |
|
| koma Yehova sadzawasiya pansi pa mphamvu yawo kapena kuti atsutsidwe pamene abweretsedwa pa milandu. |
|
| 34 |
|
| Khulupirira Yehova, ndipo sunga njira yake; Iye adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako; udzaona anthu oyipa akuwonongeka. |
|
| 35 |
|
| Ine ndinaona munthu woyipa ndi munthu wopanda chifundo akupeza bwino ngati mtengo wobiriwira pa nthaka ya makolo ake. |
|
| 36 |
|
| Koma sanachedwe kumwalira ndipo sanaonekenso; ngakhale ndinamuyangʼanayangʼana, sanapezekenso. |
|
| 37 |
|
| Ganizira za munthu wosalakwa, yangʼanitsitsa munthu wolungama; udzaona kuti ali ndi tsogolo labwino ndipo ali ndi zidzukulu zambiri. |
|
| 38 |
|
| Koma anthu ochimwa adzawonongeka; iwowo pamodzi ndi zidzukulu zawo zomwe. |
|
| 39 |
|
| Chipulumutso cha olungama chimachokera kwa Yehova; Iye ndiye linga lawo pa nthawi ya masautso. |
|
| 40 |
|
| Yehova amawathandiza ndi kuwalanditsa; Iye amawalanditsa kwa oyipa ndi kuwapulumutsa, pakuti amathawira kwa Iye. |
|
|
|
|