|
| 1 |
|
| Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu: Ndipo musandilange moopsa m'mtima mwanu. |
|
| 2 |
|
| Pakuti mibvi yanu yandilowa, Ndi dzanja lanu landigwera. |
|
| 3 |
|
| Mumnofu mwanga mulibe camoyo cifukwa ca ukali wanu; Ndipo m'mafupa anga simuzizira, cifukwa ca colakwa canga. |
|
| 4 |
|
| Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga: Ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera. |
|
| 5 |
|
| Mabala anga anunkha, adaola, Cifukwa ca kupusa kwanga. |
|
| 6 |
|
| Ndapindika, ndawerama kwakukuru; Ndimayenda woliralira tsiku lonse. |
|
| 7 |
|
| Pakuti m'cuuno mwanga mutentha kwambiri; Palibe pamoyo m'mnofu mwanga, |
|
| 8 |
|
| Ndafoka ine, ndipo ndacinjizidwa: Ndabangula cifukwa ca kumyuka mtima wanga. |
|
| 9 |
|
| Ambuye, cikhumbo canga conse ciri pamaso panu; Ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu. |
|
| 10 |
|
| Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yacoka: Ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandicokera. |
|
| 11 |
|
| Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga; Ndipo anansi anga aima patali. |
|
| 12 |
|
| Ndipo andichera misampha iwo akufuna moyo wanga; Ndipo iwo akuyesa kundicitira coipa alankhula zoononga, Nalingirira zonyenga tsiku lonse. |
|
| 13 |
|
| Koma ine, monga gonthi, sindimva; Ndipo monga munthu wosalankhula, sinditsegula pakamwa panga. |
|
| 14 |
|
| Inde ndikunga munthu wosamva, Ndipo m'kamwa mwanga mulibe makani. |
|
| 15 |
|
| Pakuti ndikuyembekezani Inu, Yehova; Inu mudzayankha, Ambuye Mulungu wanga. |
|
| 16 |
|
| Pakuti ndinati, Asakondwerere ine: Pakuterereka phazi langa, asadzikuze pa ine. |
|
| 17 |
|
| Ndafikana potsimphina; Ndipo cisoni canga ciri pamaso panga cikhalire. |
|
| 18 |
|
| Pakuti ndidzafotokozera mphulupulu yanga; Nditenga nkhawa cifukwa ca chimo langa. |
|
| 19 |
|
| Koma adani anga ali ndi moyo, nakhalandi mphamvu: Ndipo akundida kopanda cifukwa acuruka. |
|
| 20 |
|
| Ndipo iwo akubwezera coipa pa cabwino Atsutsana nane, popeza nditsata cabwino. |
|
| 21 |
|
| Musanditaye, Yehova: Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine. |
|
| 22 |
|
| Fulumirani kundithandiza, Ambuye, cipulumutso canga. |
|
|
|
|