Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, Kuti ndingacimwe ndi lilime langa: Ndidzasunga pakamwa panga ndi cam'kamwa, Pokhala woipa ali pamaso panga. |
| 2 |
| Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala cete osalawa cokoma; Ndipo cisoni canga cinabuka. |
| 3 |
| Mtima wanga unatentha m'kati mwaine; Unayaka moto pakulingirira ine: Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa: |
| 4 |
| Yehova, mundidziwitse cimariziro canga, Ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati; Ndidziwe malekezero anga, |
| 5 |
| Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; Ndipo zaka zanga ziri ngati cabe pamaso panu: Indedi munthu ali yense angakhale wokhazikika, ali cabe konse. |
| 6 |
| Indedi munthu ayenda ngati mthunzi: Indedi abvutika cabe: Asonkhanitsa cuma, ndipo sadziwa adzacilandira ndani? |
| 7 |
| Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira ciani? Ciyembekezo canga ciri pa Inu. |
| 8 |
| Ndipulumutseni kwa zolakwa zangazonse: Musandiike ndikhale cotonza ca wopusa. |
| 9 |
| Ndinakhala du, sindinatsegula pakamwa panga; Cifukwa inu mudacicita. |
| 10 |
| Mundicotsere cobvutitsa canu; Pandithera ine cifukwa ca kulanga kwa dzanja lanu. |
| 11 |
| Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula cifukwa ca mphulupulu, Mukanganula kukongola kwace monga mumacita ndi kadzoce: Indedi, munthu ali yense ali cabe. |
| 12 |
| Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo cherani khutu kulira kwanga; Musakhale cete pa misozi yanga: Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, Wosakhazikika, monga makolo anga onse. |
| 13 |
| Ndiloleni, kuti nditsitsimuke, Ndisanamuke ndi kukhala kuli zi. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/039.mp3
150
39