Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide. Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu, Inu Mulungu wa chilungamo changa. Pumulitseni ku zowawa zanga; chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa. |
| 2 |
| Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi? Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza? Sela. |
| 3 |
| Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika; Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana. |
| 4 |
| Kwiyani koma musachimwe; pamene muli pa mabedi anu, santhulani mitima yanu ndi kukhala chete. Sela |
| 5 |
| Perekani nsembe zolungama ndipo dalirani Yehova. |
| 6 |
| Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?” Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova. |
| 7 |
| Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano. |
| 8 |
| Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha, Inu Yehova, mumandisamalira bwino. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/004.mp3
150
4