Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso. |
| 2 |
| Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake. |
| 3 |
| Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda. |
| 4 |
| Ndinati, “Inu Yehova, mundichitire chifundo; chiritseni pakuti ndakuchimwirani.” |
| 5 |
| Adani anga mwankhwidzi amanena za ine kuti, “Kodi munthu ameneyu adzafa liti kuti ayiwalike?” |
| 6 |
| Pamene wina abwera kudzandiona, amayankhula mwachinyengo, pomwe mtima wake ukusonkhanitsa zachipongwe; kenaka iye amatuluka ndi kukalengeza kunja. |
| 7 |
| Adani anga onse amanongʼonezana pamodzi kulimbana nane, iwo amalingalira zoyipa kwambiri za ine, ponena kuti, |
| 8 |
| “Matenda owopsa amugwira; sadzaukapo pamalo pamene wagona.” |
| 9 |
| Ngakhale bwenzi langa la pamtima amene ndinamudalira, iye amene amadya pamodzi ndi ine watukula chidendene chake kulimbana nane. |
| 10 |
| Koma Yehova mundichititre chifundo, dzutseni kuti ndiwabwezere. |
| 11 |
| Ine ndikudziwa kuti mukukondwera nane, pakuti mdani wanga sandigonjetsa. |
| 12 |
| Mu ungwiro wanga Inu mumandisunga ndi kundiyimika pamaso panu kwamuyaya. |
| 13 |
| Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli kuchokera muyaya mpaka muyaya. Ameni ndi Ameni. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/041.mp3
150
41