×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 42

1
Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; Motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.
2
Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo: Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
3
Misozi yanga yakhalangati cakudya canga, Usana ndi usiku; Pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
4
Ndizikumbukila izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, Pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu, Ndinawatsogolera ku nyumba ya Mulungu, ndi mau akuyimbitsa ndi kuyamika, Ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
5
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso Cifukwa ca cipulumutso ca nkhope yace.
6
Mulungu wanga, moyo wanga Udziweramira m'kati mwanga; Cifukwa cace ndikumbukila Inu m'dziko la Yordano, Ndi mu Ahermone, m'kaphiri ka Mizara.
7
Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, Pa mkokomo wa matiti anu: Mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.
8
Koma usana Yehova adzalamulira cifundo cace, Ndipo usiku Nyimbo yace idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Yehova wa moyowanga.
9
Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala cifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira Cifukwa ca kundipsinja mdaniyo?
10
Adani anga andinyoza ndi kundityola mafupa anga; Pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?
11
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, Ndiye cipulumutso ca nkhope yanga ndi Mulungu wanga,
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba