Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda cifundo: Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama. |
| 2 |
| Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji? Ndimayenderanji woliralira cifukwa ca kundipsinja mdani? |
| 3 |
| Tumizirani kuunika kwanu ndi coonadi canu zinditsogolere: Zindifikitse ku phiri lanu loyera, Kumene mukhala Inuko. |
| 4 |
| Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, Kufikira Mulungu wa cimwemwe canga ceniceni: Ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga. |
| 5 |
| Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, Ndiye cipulumutso ca nkhope yanga, ndi Mulungu wanga. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/043.mp3
150
43