1
Mtima wanga wadzaza ndi nkhani yokoma. Ndikuimbira mfumu nyimbo yangayi. Lilime langa lili ngati cholembera cha katswiri wodziŵa kulemba bwino.
2
Inu ndinu wokongola kwambiri kuposa anzanu ena onse. Pakamwa panu pamatulutsa zokoma zokhazokha. Nchifukwa chake Mulungu wakudalitsani mpaka muyaya.
3
Inu ngwazi yolimba mtima, mangirirani lupanga lanu m'chiwuno, mu ulemerero ndi ukulu wanu.
4
Pitani ndi ulemerero wanuwo, kuti mukagonjetse adani anu onse, mukateteze zimene zili zoona, zachifatso ndi zachilungamo. Dzanja lanu lamanja likaonetse ntchito zanu zoopsa.
5
Mivi yanu ndi yakuthwa, imalasa mitima ya adani. Mitundu ina ya anthu imagwa pansi pamaso panu.
6
Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, ndi wamuyaya, mumaweruza molungama mu ufumu wanu.
7
Mumakonda chilungamo ndipo mumadana ndi zoipa. Nchifukwa chake Mulungu, Mulungu wanu, wakusankhani. Wakudzozani ndi kukusangalatsani kupambana anzanu ena onse.
8
Zovala zanu nzonunkhira mure, aloe ndi kasiya. Nyumba zanu zachifumu nzomangidwa ndi mnyanga. M'menemo zoimbira zansambo zimakusangalatsani,
9
ana aakazi a mafumu ali m'gulu la mbumba zanu zolemekezeka. Ku dzanja lanu lamanja kwaima mfumukazi, yovala zovala za golide wa ku Ofiri.
10
Tsono mvera kuno, mkwati wamkaziwe, imva mau anga ndipo uŵaganizire bwino. Iŵala abale ako ndiponso nyumba ya bambo wako.
11
Mfumu idzakukonda chifukwa cha kukongola kwako. Umuŵeramire popeza kuti ndiye mbuyako.
12
Anthu a ku Tiro adzakukopa ndi mphatso, olemera kwambiri adzakunyengerera
13
ndi chuma chao chamitundumitundu. Mwana wamkazi wa mfumu ali m'chipinda mwake, wadzikongoletsa kwambiri, wavala zovala zoluka ndi thonje lagolide.
14
Akupita naye kwa mfumu atavala zovala zamaluŵa, pamodzi ndi anamwali anzake omperekeza.
15
Akuŵaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo pokaloŵa m'nyumba ya mfumu.
16
Inutu zidzukulu zanu zidzaloŵa m'malo mwa makolo anu, mudzaŵasandutsa mafumu pa dziko lonse lapansi.
17
Ndidzamveketsa mbiri ku mibadwo yonse, nchifukwa chake mitundu ya anthu idzakutamandani mpaka muyaya.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi