Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali. Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto. |
| 2 |
| Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja, |
| 3 |
| ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu, ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake. |
| 4 |
| Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu, malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako. |
| 5 |
| Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa; Mulungu adzawuthandiza mmawa. |
| 6 |
| Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa; Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka. |
| 7 |
| Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu. |
| 8 |
| Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova, chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi. |
| 9 |
| Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo; amatentha zishango ndi moto. |
| 10 |
| Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu; ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu; ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.” |
| 11 |
| Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/046.mp3
150
46