Buku Loyera
|
| 1 |
| Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. |
| 2 |
| Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama, |
| 3 |
| ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma. Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja. |
| 4 |
| Koma kuli mtsinje umene mifuleni yake imasangalatsa anthu amumzinda wa Mulungu, malo oyera okhalako Wopambanazonse. |
| 5 |
| Mulungu ali m'kati mwa mzindawo, sudzaonongeka konse. Mulungu adzauthandiza dzuŵa lisanatuluke. |
| 6 |
| Mitundu ya anthu ikunjenjemera kwambiri, maufumu akugwedezeka, Mulungu akalankhula mau ake, dziko lapansi likusungunuka. |
| 7 |
| Chauta Wamphamvuzonse ali nafe. Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. |
| 8 |
| Bwerani kuti muwone ntchito za Chauta, m'mene amachitira zozizwitsa pa dziko lapansi. |
| 9 |
| Amaletsa nkhondo mpaka ku mathero a dziko lapansi. Amathyola uta, ndi kupokonyola mkondo. Amatentha magaleta ankhondo ndi moto. |
| 10 |
| “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” |
| 11 |
| Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/046.mp3
150
46