Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Nyimbo. Salimo la ana a Kora. Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera. |
| 2 |
| Lokongola mu utali mwake, chimwemwe cha dziko lonse lapansi. Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni, mzinda wa Mfumu yayikulu. |
| 3 |
| Mulungu ali mu malinga ake; Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo. |
| 4 |
| Pamene mafumu anasonkhana pamodzi, pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe, |
| 5 |
| iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri; anathawa ndi mantha aakulu. |
| 6 |
| Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera, ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira. |
| 7 |
| Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa. |
| 8 |
| Monga momwe tinamvera, kotero ife tinaona mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse, mu mzinda wa Mulungu wathu. Mulungu adzawuteteza kwamuyaya. |
| 9 |
| Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu, ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika. |
| 10 |
| Monga dzina lanu, Inu Mulungu, matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo. |
| 11 |
| Phiri la Ziyoni likukondwera, midzi ya Yuda ndi yosangalala chifukwa cha maweruzo anu. |
| 12 |
| Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo, werengani nsanja zake. |
| 13 |
| Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake, penyetsetsani malinga ake, kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira. |
| 14 |
| Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha; Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/048.mp3
150
48