×

Buku Loyera

MASALIMO 48

1
Chauta ndi wamkulu, ndi woyenera kumutamanda kwambiri. Timuyamike mu mzinda wake, pa phiri lake loyera,
2
mzinda wokongola wa Ziyoni pa phiri la Mulungu, wopatsa chimwemwe ku dziko lonse lapansi. Mzinda wa Ziyoni umene uli kumpotowu, ndi mzinda wa Mfumu yathu yaikulu.
3
Mulungu waonetsa kuti ndiye woteteza mzindawo, pakuti Iye amakhala m'kati mwa malinga ake.
4
Mafumu adasonkhana, adafuna kuuthira nkhondo pamodzi.
5
Atangopenya mzindawo adadzidzimuka, adachita mantha, nathaŵa chinambalala.
6
Adanjenjemera koopsa, ndipo adamva ululu wonga wa mkazi wovutika pa nthaŵi yochira.
7
Inu Mulungu mudaŵaononga, monga momwe mphepo yakuvuma ija imapasulira zombo zopita ku Tarisisi.
8
Zimene ife tidazimva, taziwona zomwezo mu mzinda wa Chauta Wamphamvuzonse, mzinda wa Mulungu wathu, umene adaukhazikitsa mpaka muyaya.
9
Tikakhala m'Nyumba mwanu, Inu Mulungu, timalingalira za chikondi chanu chosasinthika.
10
Inu Mulungu, anthu amakutamandani ponseponse, monga dzina lanu latchuka pa dziko lonse lapansi. Dzanja lanu lamphamvu limapambana nthaŵi zonse.
11
Anthu okhala mu Ziyoni akondwe. A ku Yuda asangalale chifukwa cha kaweruzidwe kanu kolungama.
12
Zungulirani Ziyoni yense, inde zungulirani mzinda wonsewo, ndipo muŵerenge nsanja zake.
13
Yang'anani bwino machemba ake, penyetsetsani malinga ake, kuti mudzathe kusimbira mbadwo wakutsogolo.
14
Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere, ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.”
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba