|
| 1 |
|
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. Imvani izi anthu a mitundu yonse; mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse, |
|
| 2 |
|
| anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika, olemera pamodzinso ndi osauka: |
|
| 3 |
|
| Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru; mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru. |
|
| 4 |
|
| Ndidzatchera khutu langa ku mwambo, ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga. |
|
| 5 |
|
| Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika, pamene achinyengo oyipa andizungulira. |
|
| 6 |
|
| Iwo amene adalira kulemera kwawo ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo? |
|
| 7 |
|
| Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu. |
|
| 8 |
|
| Dipo la moyo ndi la mtengowapatali, palibe malipiro amene angakwanire, |
|
| 9 |
|
| kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya ndi kusapita ku manda. |
|
| 10 |
|
| Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira; opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena. |
|
| 11 |
|
| Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya, malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo, ngakhale anatchula malo mayina awo. |
|
| 12 |
|
| Ngakhale munthu akhale wachuma chotani, adzafa ngati nyama. |
|
| 13 |
|
| Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha, ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula. Sela |
|
| 14 |
|
| Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda, ndipo imfa idzawadya. Olungama adzawalamulira mmawa; matupi awo adzavunda mʼmanda, kutali ndi nyumba zawo zaufumu. |
|
| 15 |
|
| Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda; ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini. |
|
| 16 |
|
| Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera, pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira; |
|
| 17 |
|
| Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira, ulemerero wake sudzapita pamodzi naye. |
|
| 18 |
|
| Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala, ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino, |
|
| 19 |
|
| iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake, amene sadzaonanso kuwala. |
|
| 20 |
|
| Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru adzafa ngati nyama yakuthengo. |
|
|
|
|