|
| 1 |
|
| Imvani izi, inu anthu a mitundu yonse. Tcherani khutu, inu nonse okhala pa dziko lapansi, |
|
| 2 |
|
| anthu otsika ndi okwera omwe, olemera ndi osauka omwe. |
|
| 3 |
|
| Zosinkhasinkha za mtima wanga zidzakhala zakuya, ndipo ndidzalankhula zanzeru. |
|
| 4 |
|
| Ndidzakupherani mwambi, ndidzamasulira tanthauzo lake poimba pangwe. |
|
| 5 |
|
| Ndichitirenji mantha pa nthaŵi yamavuto pamene anthu ondizunza akundizinga. |
|
| 6 |
|
| Anthu otero amangokhulupirira chuma chao, amanyada chifukwa ali ndi chuma chambiri. |
|
| 7 |
|
| Zoonadi, palibe munthu amene angadziwombole, kapena kupatsa Mulungu mtengo wa moyo wake. |
|
| 8 |
|
| Popeza kuti choombolera moyo wa munthu ndi chamtengowapatali, ndipo sangathe kuchikwanitsa, |
|
| 9 |
|
| kuti azikhalabe ndi moyo mpaka muyaya osapita ku manda. |
|
| 10 |
|
| Zoonadi, aliyense atha kuwona kuti ngakhale anthu anzeru amafa. Chimodzimodzi, anthu opusa ndi opulukira ayenera kufa ndi kusiyira ena chuma chao. |
|
| 11 |
|
| Manda ao ndiye kwao mpaka muyaya, ndi malo odzakhalako pa mibadwo yonse, ngakhale akadali moyo ankatcha maiko maina ao. |
|
| 12 |
|
| Ngakhale munthu akhale wolemera chotani, komabe adzafa chabe ngati nyama zakuthengo. |
|
| 13 |
|
| Zimenezi ndizo zimene zimaŵagwera anthu amene ali ndi chikhulupiriro chopusa, ndiwo mathero ake a onse amene amatsata maganizo otere. |
|
| 14 |
|
| Ayenera kupita ku dziko la akufa ngati nkhosa, ndipo imfa idzakhala mbusa wao. Anthu olungama adzaŵapambana. Adzatsika kulunjika ku manda, matupi ao adzaola, kwao kudzakhala kumanda. |
|
| 15 |
|
| Koma Mulungu adzaombola moyo wanga ku ulamuliro wa manda, sindidzaopa, pakuti Iye adzandilandira. |
|
| 16 |
|
| Usavutike munthu wina akamalemera, pamene chuma cha m'nyumba mwake chikukulirakulira. |
|
| 17 |
|
| Chifukwa pamene munthuyu amwalira, sadzatengapo kanthu. Chuma chake sichidzapita naye limodzi. |
|
| 18 |
|
| Ngakhale pamene munthuyo ali moyo, amadziyesa wodala, ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino, |
|
| 19 |
|
| adzafabe nkukakumana ndi makolo ake onse kumanda, kumene sadzaona kuŵala mpaka muyaya. |
|
| 20 |
|
| Ngakhale munthu akhale wolemera chotani, komabe akasoŵa nzeru, adzafa chabe ngati nyama zakuthengo. |
|
|
|
|