Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe zoyimbira za zitoliro. Salimo la Davide. Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova, ganizirani za kusisima kwanga |
| 2 |
| Mverani kulira kwanga kofuna thandizo, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera. |
| 3 |
| Mmawa, Yehova mumamva mawu anga; Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu ndi kudikira mwachiyembekezo. |
| 4 |
| Inu si Mulungu amene mumasangalala ndi zoyipa; choyipa sichikhala pamaso panu. |
| 5 |
| Onyada sangathe kuyima pamaso panu; Inu mumadana ndi onse ochita zoyipa. |
| 6 |
| Mumawononga iwo amene amanena mabodza; anthu akupha ndi achinyengo, Yehova amanyansidwa nawo. |
| 7 |
| Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu, ndidzalowa mʼNyumba yanu; mwa ulemu ndidzaweramira pansi kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera. |
| 8 |
| Tsogolereni Inu Yehova, mwa chilungamo chanu chifukwa cha adani anga ndipo wongolani njira yanu pamaso panga. |
| 9 |
| Palibe mawu ochokera mʼkamwa mwawo amene angadalirike; mtima wawo wadzaza ndi chiwonongeko. Kummero kwawo kuli ngati manda apululu; ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo. |
| 10 |
| Lengezani kuti ndi olakwa, Inu Mulungu! Zochita zawo zoyipa zikhale kugwa kwawo. Achotseni pamaso panu chifukwa cha machimo awo ambiri, pakuti awukira Inu. |
| 11 |
| Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere; lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe. Aphimbeni ndi chitetezo chanu, iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu. |
| 12 |
| Ndithu, Inu Yehova, mumadalitsa olungama; mumawazungulira ndi kukoma mtima kwanu ngati chishango. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/005.mp3
150
5