|
| 1 |
|
| Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, Aitana dziko lapansi kuyambira kuturuka kwa dzuwa kufikira kulowa kwace. |
|
| 2 |
|
| Mulungu awalira m'Ziyoni, mokongola mwangwiro. |
|
| 3 |
|
| Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala cete: Moto udzanyeka pankhope pace, Ndipo pozungulira pace padzasokosera kwakukuru. |
|
| 4 |
|
| Kumwamba adzaitana zakumwamba, Ndi dziko lapansi, kuti aweruze anthu ace: |
|
| 5 |
|
| Mundisonkhanitsire okondedwa anga; Amene anapangana ndi Ine ndi nsembe. |
|
| 6 |
|
| Ndipo zakumwamba zionetsera cilungamo cace; Pakuti Mulungu mwini wace ndiye woweruza. |
|
| 7 |
|
| Imvani, anthu anga, ndipo ndidzanena; Israyeli, ndipo ndidzacita mboni pa iwe: Ine Mulungu, ndine Mulungu wako. |
|
| 8 |
|
| Sindikudzudzula iwe cifukwa ca nsembe zako; Popeza nsembe zako zopsereza ziri pamaso panga cikhalire. |
|
| 9 |
|
| Sindidzatenga ng'ombe m'nyumbamwako, Kapena mbuzi m'makola mwako. |
|
| 10 |
|
| Pakuti zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga, Ndi ng'ombe za pa mapiri zikwi. |
|
| 11 |
|
| Ndidziwa mbalame zonse za m'mapiri: Ndipo nyama za kuthengo ziri ndi Ine. |
|
| 12 |
|
| Ndikamva njala, sindidzakuuza: Pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwace komwe. |
|
| 13 |
|
| Kodi ndidzadya nyama ya ng'ombe, Kapena kumwa mwazi wa mbuzi? |
|
| 14 |
|
| Pereka kwa Mulungu nsembe yaciyamiko; Numcitire Wam'mwambamwamba cowinda cako: |
|
| 15 |
|
| Ndipo undiitane tsiku la cisautso: Ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza. |
|
| 16 |
|
| Koma kwa woipa Mulungu anena, Uli nao ciani malemba anga kulalikira, Ndi kuchula pangano langa pakamwa pako? |
|
| 17 |
|
| Popeza udana naco cilangizo, Nufulatira mau anga. |
|
| 18 |
|
| Pakuona mbala, ubvomerezana nayo, Nucita nao acigololo. |
|
| 19 |
|
| Pakamwa pako mpocita zocimwa, Ndipo lilime lako likonza cinyengo. |
|
| 20 |
|
| Ukhala, nuneneza mbale wako; Usinjirira mwana wa mai wako. |
|
| 21 |
|
| Izi unazicita iwe, ndipo ndinakhala cete Ine; Unayesa kuti ndifanana nawe: Ndidzakudzudzula, ndi kucilongosola pamaso pako. |
|
| 22 |
|
| Dziwitsani ici inu oiwala Mulungu, Kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi: |
|
| 23 |
|
| Wopereka nsembe yaciyamiko andilemekeza Ine; Ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ace Ndidzamuonetsa cipulumutso ca Mulungu. |
|
|
|
|