|
| 1 |
|
| Salimo la Asafu. Wamphamvuyo, Yehova Mulungu, akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera. |
|
| 2 |
|
| Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri Mulungu akuwala. |
|
| 3 |
|
| Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete; moto ukunyeketsa patsogolo pake, ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho |
|
| 4 |
|
| Iye akuyitanitsa zamumlengalenga ndi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake. |
|
| 5 |
|
| Mundisonkhanitsire okhulupirika anga, amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe. |
|
| 6 |
|
| Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake, pakuti Mulungu mwini ndi woweruza. |
|
| 7 |
|
| Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula, iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa; ndine Mulungu, Mulungu wako. |
|
| 8 |
|
| Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako, kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse. |
|
| 9 |
|
| Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lako kapena mbuzi za mʼkhola lako, |
|
| 10 |
|
| pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yanga ndiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka. |
|
| 11 |
|
| Ine ndimadziwa mbalame iliyonse mʼmapiri ndiponso zolengedwa zonse zakutchire ndi zanga. |
|
| 12 |
|
| Ndikanakhala ndi njala sindikanakuwuzani, pakuti dziko lonse ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndi zanga. |
|
| 13 |
|
| Kodi ndimadya nyama ya ngʼombe zazimuna kapena kumwa magazi a mbuzi? |
|
| 14 |
|
| “Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu, kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba. |
|
| 15 |
|
| Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso; Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.” |
|
| 16 |
|
| Koma kwa woyipa, Mulungu akuti, “Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga kapena kutenga pangano langa pa milomo yako? |
|
| 17 |
|
| Iwe umadana ndi malangizo anga ndipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga. |
|
| 18 |
|
| Ukaona wakuba umamutsatira, umachita maere ako pamodzi ndi achigololo |
|
| 19 |
|
| Umagwiritsa ntchito pakamwa pako pa zinthu zoyipa ndipo umakonza lilime lako kuchita chinyengo. |
|
| 20 |
|
| Nthawi zonse umayankhula motsutsana ndi mʼbale wako ndipo umasinjirira mwana wa amayi ako enieni. |
|
| 21 |
|
| Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete; umaganiza kuti ndine wofanana nawe koma ndidzakudzudzula ndipo ndidzakutsutsa pamaso pako. |
|
| 22 |
|
| “Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa: |
|
| 23 |
|
| Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza, ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse chipulumutso cha Mulungu.” |
|
|
|
|