×

Buku Loyera

MASALIMO 50

1
Chauta, Mulungu Wamphamvu uja, akulankhula, akuitana anthu a ku dziko lonse lapansi, kuyambira kotulukira dzuŵa mpaka koloŵera kwake.
2
Mulungu akuŵala atakhala m'Ziyoni, mzinda wake wokongola kotheratu.
3
Mulungu wathu akubwera, sakhala chete. Patsogolo pake pali moto wonyeketsa, M'mbali mwake monse muli mkuntho wamphamvu.
4
Amaitana zamumlengalenga ndi za pansi pano, kuti zichite umboni pamene akuweruza anthu ake.
5
Iye akuti, “Sonkhanitsani pamaso panga, anthu anga okhulupirika, amene adachita chipangano ndi Ine popereka nsembe.”
6
Zamumlengalenga zikulalika chilungamo cha Mulungu, pakuti Iye mwini ndiye muweruzi.
7
“Imvani anthu anga, Ine ndidzalankhula. Ndidzapereka umboni wokutsutsani inu Aisraele. Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.
8
“Sindikudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu, popeza kuti mumapereka nsembe zanu zopsereza kwa Ine nthaŵi zonse.
9
Ndithudi, sindilandira ng'ombe kapena mbuzi iliyonse ya m'makola anu.
10
“Popeza kuti nyama iliyonse yam'nkhalango ndi yanga, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku mapiri ochuluka.
11
Mbalame zonse zamumlengalenga, zamoyo zonse zoyenda ku thengo ndi zanga.
12
“Ndikadakhala ndi njala sindikadakuuzani, pakuti dziko lonse ndi zonse zam'menemo, ndi zanga.
13
Kodi ndimadya nyama yang'ombe kapena magazi ambuzi?
14
“Koma perekani nsembe zanu zothokozera kwa Mulungu, ndipo muchite zimene mudalumbira kwa Wopambanazonse.
15
Mupemphere kwa Ine pa tsiku lamavuto. Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”
16
Koma kwa munthu woipa Mulungu amati, “Ukuvutikiranji ndi kutchula malamulo anga? Bwanji pakamwa pako pakulankhula za chipangano changa?
17
Iwe sufuna kulangizidwa, umaponya mau anga ku nkhongo.
18
“Ukaona mbala umasanduka bwenzi lake, ndipo umayenda ndi anthu achigololo.
19
Suwopa kulankhula zoipa pakamwa pako, lilime lako limapeka mabodza.
20
“Umakhala pansi nkumachitira mbale wako miseche, inde, umasinjirira mbale wako weniweni.
21
Iwe wachita zinthu zimenezi, ndipo Ine ndakhala ndili chete. Unalikuganiza kuti ndimafanafana nawe. Koma tsopano ndikukudzudzula ndi kukuwonetsa zimene wachita.
22
“Ganizani bwino izi tsono, inu amene mumaiŵala Mulungu, kuti ndingakukadzuleni, ndipo palibe amene angakupulumutseni.
23
Koma wopereka mtima wake kwa Ine mothokoza, ndiye amene amandilemekeza. Woyenda m'njira zolungama, ndidzamuwonetsa chipulumutso changa.”
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba