Buku Loyera
|
| 1 |
| Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino. |
| 2 |
| Mulungu kumwambako waŵerama, akuyang'ana anthu pansi pano, kuti aone ngati angakhalepo mmodzi wanzeru wofunitsitsa Mulungu. |
| 3 |
| Koma ai anthu onse ndi osokera, onsewo ndi oipa chimodzimodzi. Palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino, ai, palibiretu ndi mmodzi yemwe. |
| 4 |
| Kani anthu oipaŵa alibe nzeru chotere? Iwo amameza anthu anga, kuŵayesa chakudya, ndipo samutama Mulungu mopemba. |
| 5 |
| Tsonotu iwo adzachita mantha aakulu, mantha ake amene sadaoneke ndi kale lonse. Pakuti Mulungu adzaononga adani okuzingani. Inu mudzaŵachititsa manyazi chifukwa Mulungu waŵakana. |
| 6 |
| Chibwere ndithu chipulumutso cha Israele kuchokera ku Ziyoni! Mulungu akadzaŵabwezera ufulu anthu ake, Yakobe adzakondwera, Israele adzasangalala kwambiri. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/053.mp3
150
53