Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Njiwa pa Mtengo wa Thundu wa Kutali.” Mikitamu ya Davide, pamene Afilisti anamugwira ku Gati. Mundichitire chifundo Inu Mulungu, pakuti anthu akundithamangitsa kwambiri; tsiku lonse akundithira nkhondo. |
| 2 |
| Ondinyoza akundithamangitsa tsiku lonse, ambiri akumenyana nane monyada. |
| 3 |
| Ndikachita mantha ndimadalira Inu. |
| 4 |
| Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda, mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha. Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani? |
| 5 |
| Tsiku lonse amatembenuza mawu anga; nthawi zonse amakonza zondivulaza. |
| 6 |
| Iwo amakambirana, amandibisalira, amayangʼanitsitsa mayendedwe anga ndipo amakhala ndi chidwi chofuna kuchotsa moyo wanga. |
| 7 |
| Musalole konse kuti athawe; mu mkwiyo wanu Mulungu mugwetse mitundu ya anthu. |
| 8 |
| Mulembe za kulira kwanga, mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu. Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo? |
| 9 |
| Adani anga adzabwerera mʼmbuyo pamene ndidzalirira kwa Inu. Pamenepo ndidzadziwa kuti Mulungu ali ku mbali yanga. |
| 10 |
| Mwa Mulungu amene mawu ake ndimawatamanda, mwa Yehova amene mawu ake ndimawatamanda, |
| 11 |
| mwa Mulungu ine ndimadalira ndipo sindidzachita mantha. Kodi munthu angandichite chiyani? |
| 12 |
| Ndiyenera kuchita zomwe ndinalumbira kwa Mulungu; ndidzapereka nsembe zanga zachiyamiko kwa inu. |
| 13 |
| Pakuti mwawombola moyo wanga ku imfa ndi mapazi anga kuti ndingagwe, kuti ndiyende pamaso pa Mulungu mʼkuwala kwa moyo. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/056.mp3
150
56