Buku Loyera
|
| 1 |
| Inu Mulungu, mundichitire chifundo, pakuti anthu akundizunza. Adani akundithira nkhondo ndi kundipsinja tsiku lonse. |
| 2 |
| Adani akundizunza tsiku lonse, pali ambiri amene akumenyana nane monyada. |
| 3 |
| Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. |
| 4 |
| Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani? |
| 5 |
| Tsiku lonse adaniwo amafunafuna kulepheretsa zolinga zanga. Zonse zimene amaganiza ndi zoti andichite zoipa. |
| 6 |
| Amasonkhana okhaokha namabisalira, amalonda mayendedwe anga, amafuna kundipha. |
| 7 |
| Muŵalange chifukwa cha zoipa zao. Inu Mulungu, muŵakwiyire anthuwo ndi kuŵaononga. |
| 8 |
| Inu mwaona kupiripita kwanga, mudziŵa kuchuluka kwa misozi yanga. Kodi zonsezi sizidalembedwe m'buku lanu? |
| 9 |
| Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu. Ndikudziŵa kuti Mulungu ali pa mbali yanga. |
| 10 |
| Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha mau ake. Ndimatamanda Chauta chifukwa cha zimene wandilonjeza. |
| 11 |
| Ndimadalira Mulungu, sindidzachita mantha konse. Kodi munthu angandichite chiyani? |
| 12 |
| Ndiyenera kuchita zimene ndidalumbira kwa Inu Mulungu. Ndidzapereka kwa Inu nsembe zothokozera. |
| 13 |
| Pakuti mwalanditsa moyo wanga ku imfa. Inde mwandichirikiza mapazi kuti ndisagwe, kuti motero ndiziyenda pamaso pa Mulungu m'kuŵala kwa amoyo. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/056.mp3
150
56