×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 57

1
Mundicitire cifundo, Mulungu, mundicitire cifundo; Pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu: Ndipo ndithawira ku mthunzi wa mapiko anu, Kufikira zosakazazo zidzapita.
2
Ndidzapfuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba; Ndiye Mulungu wonditsirizira zonse.
3
Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa Ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza cifundo cace ndi coonadi cace.
4
Moyo wanga uli pakati pa mikango; Ndigona pakati pa oyaka moto, Ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mibvi, Ndipo lilime lao ndilio lupanga lakuthwa.
5
Mukwezeke m'mwambamwa mba, Mulungu; Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6
Anandichera ukonde apo ndiyenda; Moyo wanga wawerama: Anandikumbira mbuna patsogolo panga; Anagwa m'kati mwace iwo okha.
7
Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; Ndidzayimba, inde, ndidzayimba zolemekeza.
8
Galamuka, ulemu wanga; galamukani cisakasa ndi zeze: Ndidzauka ndekha mamawa.
9
Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye: Ndidzakuyimbirani mwa mitundu.
10
Pakuti cifundo canu ncacikuru kufikira m'mwamba, Ndi coonadi canu kufikira mitambo.
11
Kwezekani m'mwambamwamba, Mulungu; Ulemerero wanu ukhale pamwamba m'dziko lonse lapansi.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba