Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide. Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, kapena kundilanga mu ukali wanu. |
| 2 |
| Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka; Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu. |
| 3 |
| Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu. Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti? |
| 4 |
| Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse; pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. |
| 5 |
| Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira; Amakutamandani ndani ali ku manda? |
| 6 |
| Ine ndatopa ndi kubuwula; usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga; ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi. |
| 7 |
| Maso anga atupa chifukwa cha chisoni; akulephera kuona chifukwa cha adani anga. |
| 8 |
| Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa, pakuti Yehova wamva kulira kwanga. |
| 9 |
| Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo; Yehova walandira pemphero langa. |
| 10 |
| Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha; adzabwerera msangamsanga mwa manyazi. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/006.mp3
150
6