Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; Mwakwiya; tibwezereni. |
| 2 |
| Mwagwedeza dziko, mwaling'amba: Konzani ming'alu yace; pakuti ligwedezeka. |
| 3 |
| Mwaonetsa anthu anu zowawa: Mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa. |
| 4 |
| Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu, Aikweze cifukwa ca coonadi. |
| 5 |
| Kuti okondedwa anu alanditsidwe, Pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutibvomereze. |
| 6 |
| Mulungu walankhula m'ciyero cace; ndidzakondwerera: Ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso cigwa ca Sukoti. |
| 7 |
| Gileadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga; Ndipo Efraimu ndi mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga, |
| 8 |
| Moabu ndiye mkhate wanga; Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga: Filistiya, pfuulatu cifukwa ca ine. |
| 9 |
| Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu? |
| 10 |
| Si ndinu, Mulungu, amene mwantaya? Osaturuka nao makamu athu, Mulungu. |
| 11 |
| Tithandizeni kunsautso; Kuti cipulumutso ca munthu ndi cabe. |
| 12 |
| Mwa Mulungu tidzacita molimbika mtima, Ndipo Iye adzapondereza otisautsa. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/060.mp3
150
60