×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 61

1
Imvani mpfuu wanga, Mulungu; Mverani pemphero langa.
2
Ku malekezero a dziko lapansi ndidzapfuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga: Nditsogolereni ku thanthwe londiposa ine m'kutalika kwace.
3
Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pathawa mdani ine.
4
Ndidzagonera-gonerabe m'cihemamwanu; Ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.
5
Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga; Munandipatsa colowa ca iwo akuopa dzina lanu.
6
Mudzatalikitsa moyo wa mfumu: Zaka zace zidzafikira mibadwo mibadwo.
7
Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu; Mumpatse cifundo ndi coonadi zimsunge.
8
Potero ndidzayimba zolemekeza dzina lanu ku nthawi zonse, Kuti ndicite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba