Buku Loyera
|
| 1 |
| Inu Mulungu, imvani kulira kwanga, mverani pemphero langa. |
| 2 |
| Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali. |
| 3 |
| Inutu ndinu kothaŵira kwanga, nsanja yolimba yonditeteza kwa adani. |
| 4 |
| Mundilole ndizikhala m'Nyumba mwanu nthaŵi zonse. Mundilole ndibisale pansi pa mapiko anu kuti munditeteze. |
| 5 |
| Inu Mulungu, mwamva zimene ndalumbira popemphera. Inu mwandipatsa choloŵa chimene amalandira anthu oopa dzina lanu. |
| 6 |
| Talikitsani moyo wa mfumu, zaka zake zifikire ku mibadwo ndi mibadwo. |
| 7 |
| Akhale pa mpando wake waufumu pamaso pa Mulungu mpaka muyaya. Inu Chauta, mumsunge mokhulupirika chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. |
| 8 |
| Motero nthaŵi zonse ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, tsiku ndi tsiku ndidzachitadi zimene ndidalumbirazo. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/061.mp3
150
61