Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Yedutuni, Salimo la Davide. Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye. |
| 2 |
| Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu. |
| 3 |
| Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti, kumupha iye, nonsenu, monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka? |
| 4 |
| Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake; akondwera nao mabodza; adalitsa ndi m'kamwa mwao, koma atemberera mumtima. |
| 5 |
| Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye. |
| 6 |
| Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka. |
| 7 |
| Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu. |
| 8 |
| Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife. |
| 9 |
| Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu akulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya. |
| 10 |
| Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu. |
| 11 |
| Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri, kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu. |
| 12 |
| Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/psalms/062.mp3
150
62