Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda. Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, moona mtima ine ndimakufunafunani; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka inu, mʼdziko lowuma ndi lotopetsa kumene kulibe madzi. |
| 2 |
| Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. |
| 3 |
| Chifukwa chikondi chanu ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani. |
| 4 |
| Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga, ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga. |
| 5 |
| Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona. Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya. |
| 6 |
| Pa bedi panga ndimakumbukira inu; ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku. |
| 7 |
| Chifukwa ndinu thandizo langa, ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu. |
| 8 |
| Moyo wanga umakangamira Inu; dzanja lanu lamanja limandigwiriziza. |
| 9 |
| Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa; adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi. |
| 10 |
| Iwo adzaperekedwa ku lupanga ndi kukhala chakudya cha ankhandwe. |
| 11 |
| Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo, koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/063.mp3
150
63